A Peter Vanasiyo, 28, achita mphumi pamene apambana K200 million pa masewero a juga otchedwa Aero amene amachititsa ndi a kampani ya BetPawa. Iwo anayikapo ndalama yokwana K200 yokha kuti achite mphumi.
A Vanasiyo ndi ochokera m’boma la Ntcheu ndipo ndi mlimi komanso amachita malonda oyendetsa Kabaza.
Poyankhula ku Blantyre pamene amalandira ndalamayi, Vanasiyo anati ndalamayi imuthandiza kuti ayambe mabizinesi osiyanasiyana kuphatikizapo bizinesi ya ulimi wa nthilira, umene anati umuthandiza kuti alembeko ntchito achinyamata a mdera lake.
Mkulu owona ntchito zamalonda ku mwera kwa Africa ku BetPawa, a Bwalya Musonda Noah, anati kampaniyi ili ndi kuthekera kolipira ndalama kwa anthu onse owina ngakhale munthu atawina ndalama zankhaninkhani.
A Noah anatsindikanso kuti anthu asamatenge juga ngati njira yopezera ndalama mwa changu koma adziyitenga ngati masewero chabe.
Olemba: Alufisha Fischer