Yemwe anali mtsogoleri wa aphungu otsutsa boma ku nyumba ya malamulo, Kondwani Nankhumwa, walengeza kuti watula pansi udindowu.
Iwo ati zikhala zovuta kupitilirabe kukhala pa udindowu pambuyo poyambitsa chipani chawo chatsopano.
Poyankhula munzinda wa Blantyre, iwo ati pakali pano awuza kale owaimira pa mlandu okhudza ofesiyi omwe uli ku bwalo lamilandu kuti awuyimitse.
Olemba: Blessings Cheleuka