Charles Sinetre ndimmodzi wa akatswiri amene adayimba limodzi ndi malemu Lucius Banda. Kodi adzamukumbukira motani? Olembankhani wathu Simeon Boyce anacheza ndi Sinetre motere:
Q-Kodi ndi Lucius Banda munadziwana bwanji?
Ine ndi Lucius Banda tinakulira limodzi kuyambira mu ubwana wathu kumudzi wa Sosola kuno ku Balaka. Kucheza kwathu kunayamba momwe amachitira ana kuti kuwasiya pamodzi amapezeka kuti akusewelera limodzi.
Ine ndi Lucius tinali anthu okonda kudya moti nthawi imeneyo tinayambitsa kalabu yomwe cholinga chake kunali kudya basi. Timati tikakhala ndi ndalama, timakagula buledi otentha ku bakery, timakhala ndi mtedza komanso chimanga ndi zina.
Q-Kodi kuyimba kunayamba bwanji ?
Ine ndi Lucius timayimbira limodzi ku tchalitchi ya katolika ku Balaka kenaka mkulu wake wa Lucius, Paul Banda, yemwe panthawi imeneyo amatsogolera gulu la Aleluya, atawona luso mwa ife, anatilimbikitsa kuti tidzikayimba mu gululi.
Lucius anali ndi luso loyimba keyboard komanso kutsogolera pomwe ine luso langa ndi loyimba mawu komanso gitala.
Ine ndi Lucius tinayimbira limodzi koyamba pamwambo olandira Papa Yohane Paulo Wachiwiri (Pope John Paul II) munzinda wa Blantyre m’chaka cha 1989. Nyimbo yomwe inatchuka nthawi imeneyo inkatchedwa kuti “Tikalandire Papa ndi Chimwemwe”.
Q-Kodi dzina loti Soja linachokera pati?
Dzina la Soja ndinampatsa ndine chifukwa nthawi zambiri ine ndikamaliza kuyimba zanga komanso zina zakunja, ndimakonda kusinthana ndi iyeyo ndiye posinthanapo ine ndimakuwa kuti ” Soja take over” ngati kumupatsira kuti atenge bwalo. Komanso nthawi imeneyo tinkavala zovala zachisilikali motengera gulu loyimba la m’dziko la South Africa la Lucky Dube linkavalira.
Q-Nthawi yomwe mumayikumbukira pakugwira ntchito kwanu ndi Lucius ndi iti?
A- Nthawi Ina yake tinakayimba ku sukulu ya za ukachenjede ya Chancellor College ku Zomba koma mwambowu sunayende bwino chifukwa kunachitika zipolowe koma m’mawa wa tsikuli pomwe ine ndi Lucius tinkafotokozerana za kukhumudwa kwathu ndi ndalama zomwe tinataya pokonza mwambowu, kunatulukira mnyamata wina yemwe anatiwuza mokondwa kuti ndi iye anayambitsa zipolowe kuti mwambowu usokonekere…izi zinandikwiyitsa moti ndinkafuna ndimuthire chibakera koma Lucius anandikhazikitsa mtima pansi.
Q-Nyimbo ya Lucius yomwe mudzayikumbuke ndi iti?
A-Son of a Poor Man…iyi ndi nyimbo yomwe ndidzayikumbukire chifukwa anayipeka pomwe anapita ku maliro koma anthu amamuseka chifukwa analibe nsapato ndiye nyimbo imakamba zachitonzo chomwe amakumana nacho chifukwa chochokera banja losauka.
Q- Tidzimukumbukira bwanji?
A- Lucius anali katswiri yemwe amatha kupitiriza luso lake loyimba komanso kumachita za ndale zonse nkumayenda bwinobwino.
Anali wa ntchito zachifundo, nthawi zambiri timati tikabwera koyimba, kunyumba kwake kumadzadza anthu odzapempha thandizo losiyanasiyana ndipo ndalama zake zonse amatha kuzimaliza kugawira anthuwa.
Iyenso anali oyankhula mwatchutchu komanso samasunga mkwiyo, mumati mukasemphana chichewa amayesetsa kupeza njira yothetsera kusemphanaku.