Bungwe la German Federal Bureau of Aircraft Accident Investigation (BFU) latulutsa lipoti la ngozi ya ndege imene inachitikira mu nkhalango ya Chikangawa m’boma la Mzimba, imene idapha wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino wakale, Dr Saulos Chilima ndi anthu ena asanu ndi atatu.
Mwazina, lipotili lati mu ndegeyo munalibemo zipangizo zotapa mawu zotchedwa Cockpit Voice Recorder, zimene malinga ndi malamulo okhudza maulendo a mlenga-lenga sizofunikira kwenikweni.
Kuonjezera apo, chipangizo chopangitsa kuti ndege ipezeke mosavuta, Emergency Transmission Locator, chinali battery limene akuti linatha m’chaka cha 2004 ndipo malinga ndi a Malawi Defence Force, palibepo ndalama imene inayikidwa pambali kuti akagule lina kapena kugula zipangizo zatsopano.
BFU idaunikanso malipoti asanu ndi atatu a akatswiri a zachipatala opima matupi amene adasonyeza kuti anthuwo adavulala kwambiri mmutu ndi pachifuwa pangozi yandegeyo.
Ngoziyi idachitika pa 10 June chaka chino ndipo panthawiyi, Dr Chilima ankafuna akakhale nawo pamwambo wa maliro a Ralph Kasambara m’boma la Nkhata Bay.