Akuluakulu oyendetsa zamasewero mchigawo chakumpoto ati akhwimitsa malamulo kuti matimu amene akusewera mu chikho cha Mzuzu FAM under 21 League akhale okhawo amene ndi achisodzera ogwirizana ndi zaka zampikisanowo. Mlembi wamkulu wa Northern Region Football Association, Masiya Nyasulu, wayankhula izi pamapeto pa chikhochi kwa Luwinga pamene timu ya socials ya Hilltop imakumana ndi timu ya Soweto yochokera ku Kafukule m’boma la Mzimba.
Iwo ati ndizomvetsa chisoni kuti mpikisano umene amayenera kuti adzisewera ndi anyamata achisodzera timu imene yapambana ndiya socials ya akuluakulu oti anasewera mpira ndipo anakula.
Mmodzi mwa nthumwi kumaseweroko Alufeyo Chipanga wapereka K200,000 yapamwamba ku timu ya Soweto yaku Kafukule komanso walonjeza kuti athandiza timuyo ndi uniform yatsopano komanso mipira ati chifukwa anabwer etsa timu yachisodzera komanso achokera dera lakumudzi.
Pamasewerowo timu ya Hilltop Socials yagonjetsa timu ya Soweto yochokera ku Kafukule m’boma la Mzimba ndi zigoli zitatu kwa du. Ndipo Mphuzitsi watimuyo Madalitso Chiumia wati kupita chitsogolo akhazikitsa timu yachisodzera kuti idzisewera mu chikhocho.
Ena mwa osewera a timu ya Hilltop ndi kuphatikizapo Mtopicho Njewa yemwe anapuma kusewera mpira mu timu ya Moyale Barracks ndi azibambo ena osiyanasiyana amene amaseweranso ma timu a socials amu Mzinda wa Mzuzu.
Timu ya Hilltop yalandira K1 million, pamene timu ya Soweto yalandira K400,000 ndi ndalama zina zapadera kuchokera kwa Alufeyo Chipanga, zokwana K200,000, Henzi Banda K100,000 komanso Masiya Nyasulu K50,000.
Olemba Hassan Phiri