Malawi Broadcasting Corporation
Nkhani

Limbikani ntchito titukule dziko lathu – Dr Usi

Wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino Dr Michael Usi wapempha anthu ogwira ntchito m’boma kuti adzigwira ntchito modzipereka pofuna kutukula dziko lino, mogwirizana ndi masomphenya a Malawi 2063.

Dr Usi ayankhula izi atayendera mwadzidzidzi ntchito zingapo zaboma m’boma la Chikwawa, kuphatikizapo chipatala cha pa boma la Chikwawa komanso maofesi a khonsolo ya bomali.

Iwo ayamikiranso bwanankubwa wa bomali, a Nardin Kamba komanso mkulu owona za umoyo m’mbomali, Dr Grace Momba, kaamba kosunga nthawi komaso kugwira ntchito modzipereka, zimene ati ndikuonetsa chitsanzo chabwino kwa anthu amene amawayang’anira.

Iwo anaimanso pa malo a zamalonda pa Thabwa pomwe anacheza ndi anthu ochita malonda osiyanasiyana.

Pakadali pano, Dr Usi abwelera munzinda wa Blantyre.

Related posts

‘Lekani kugwilira ana’

Romeo Umali

Bungwe la MEC lalowa mu mgwirizano obwerekana katundu ndi bungwe la ECZ

Romeo Umali

Wagona ndi mwana komanso kuponya zithunzi zake zolaula pa Facebook

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.