Aphunzitsi ndi anthu ena oyang’anira ana awachenjeza kuti alekeletu mchitidwe ogwilira ana kupanda kutero lamulo ligwira ntchito.
M’modzi mwa akuluakulu ku unduna oona kuti pasamakhale kusiyana pakati pa amayi ndi abambo, a Chikondi Chiumbudzo Mponda, apereka chenjezoli pamwambo opereka masatifiketi kwa alezi amene amaliza maphunziro awo pansi pampingo wa CCAP Livingstonia Synod m’boma la Mzimba.
A Mponda ati ndi zomvetsa chisoni kuti m’malo moyang’anira ana, aphunzitsi ena akumawagwilira zimene anati ndi zobwezera m’mbuyo ntchito yoteteza ana.
“Posachedwapa aphunzitsi atatu amangidwa chifukwa chogwilira ana, izi ndi zodandaulitsa chifukwa anawa amakhala m’manja mwawo ndipo boma sililekelera mchitidwe otero,” a Mponda anatero.
Mkulu oona za maphunziro a m’mera mpoyamba ku nthambi yampingo wa CCAP Livingstonia Synod, Reverend Nancy Chunga, anati ngakhale pali zovuta zina, ntchito yolimbikitsa maphunziro a m’mera n’poyamba ikuyenda bwino kumpingowu.
Olemba: Henry Haukeya