Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

Adindo a NEEF akukambirana ndi Dr Usi

Wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino, Dr Michael Usi, m’mawa uno akukambirana ndi adindo a bungwe lokongoza ndalama zochitira malonda la NEEF.

Zokambiranazi zikuchitikira ku ofesi ya Dr Usi ku Capital Hill mu mzinda wa Lilongwe.

Mkumanowu ukuchitika pamene bungwe la NEEF lalimbikitsa ntchito yofikila anthu osiyanasiyana maka amayi ndi achinyamata kuti azipeza mwayi wa ngongole mosavuta.

Sabata yathayi, NEEF idakhazikitsa ndondomeko yoti wachinyamata aliyense atha kutemga ngongole ya K1 million popanda kupereka chikole chilichonse ku NEEF, ngati njira yoti anyamata ambiri atenge ngongole n’kumakhala odzidalira pa chuma.

Related posts

Zomba ready for e-payment system

Romeo Umali

Habitual thief sentenced to eight years in jail

Romeo Umali

Malawi’s life expectancy improves despite COVID-19 pandemic

Romeo Umali
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.