Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

GESD yayamba kumanga mlatho wa Limbe

Ndondomeko ya chitukuko ya GESD ikumanga mlatho wa Limbe wa ndalama zokwana K200 million zomwe zithandize m’midzi ya Kadzuwa m’dera la Inkosi Bvumbwe m’boma la Thyolo ndi Chadzunda m’boma la Blantyre, pamene pamadutsa mtsinje wa Limbe omwenso ndi malire a mabomawa.

Bwanankubwa wa boma la Thyolo, a Hudson Kuphanga, ati mlathowo ndi ofunika kwambiri potukula chuma cha anthu a m’deralo omwe amalima mbewu zosiyanasiyana.

“Anthuwa akhala akuvutika mayendedwe akatenga katundu kupita naye ku msika. Mlathowu upangitsa kuti adzikwera magalimoto,” a Kuphanga anatero.

Phungu wa dera la kumpoto kwa boma la Thyolo, a Ephraim Nayeja, anati anthu a m’deralo kuphatikizapo mafumu ndi okondwa ndi chitukukocho chomwe chatenga nthawi yaitali kuti chiyambe.

“Papita zaka zoposa 45 kuchoka pomwe anthu a m’dera lino anapempha mlathowu ku boma. Izitu ndi zopereka chilimbikitso pa chitukuko,” anatero a Nayeja.

 

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

All set for 2024 National Youth Summit – NYCOM

Olive Phiri

Nsanje District Council wants agricultural infrastructure in community plans

MBC Online

Gaba strikes again for Moroka

Stephen Dakalira
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.