Anthu ochuluka akhamukira ku bwalo lamasewero la pa msika wa Area 24 ku Lilongwe komwe kukhale msonkhano wa chipani cha Malawi Congress (MCP).
Pakadali pano, zokonzekera zonse zatha pamene anthu akudikira mtsogoleri wadziko lino Dr Lazarus Chakwera kuti adzakhale nawo pa msonkhanowu.
Magule osiyanasiyana akuvinidwaa ndipo oyimba monga Skeffa Chimoto komanso Mlaka Maliro akusangalatsa anthu.
Akuluakulu achipani, aphungu anyumba yamalamulo, mafumu a m’boma la Lilongwe, anyamata, asungwana komanso amayi ndi abambo adzadza pa bwalo la Maseweroli.