Malawi Broadcasting Corporation
Local Local News Nkhani

Kamang’aleni akakuchitirani nkhanza — Mfumu Mwamlowe

Mfumu yayikilu Mwamlowe ya m’boma la Rumphi yadandaula ndi m’chitidwe wa anthu amene sabwera poyera akachitiridwa nkhanza ndipo yati pakufunika kupeza njira mwansanga zothetsa m’chitidwewu.

Mfumuyi yanena izi ku Chiweta m’boma la Rumphi pamwambo okumbukira masiku 16 othana ndi nkhanza padziko lonse umene bungwe la Rumphi Women Forum linakonza mothandizana ndi Action Aid Malawi.

Mkulu wabungwe la Rumphi Women Forum, a Chiza Ngulube, anati anakonza mwambowu poona nkhanza zimene dera la Mwamlowe limakumana nazo.

M’modzi mwa akuluakulu aku ofesi yoona zakuti pasamakhale kusiyana pa ntchito pakati pa amuna ndi akazi m’boma la Rumphi, a Atupele Mwalweni, anapempha mabungwe kuti apitirize kuzindikiritsa anthu zakuyipa kwa nkhanza ngakhale masiku 16 okumbukira kuthana ndi nkhanza tsopano atha.

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Tiyeni tiphunzirepo pa moyo wa Dr. Chilima – St Patrick’s Parish

MBC Online

Man commits suicide over life challenges

Romeo Umali

Chakwera to arrive in BT

Eunice Ndhlovu
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.