Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

Kalembera wa voti ali mkati

Ntchito yolemba mayina a anthu m’kaundula wa voti ili mkati pa sukulu ya pulayimare ya Manja ku Blantyre.

Pamene MBC inayendera pa malowa inapeza kuti anthu ambiri akubwera kudzalembetsa mayina awo m’kaundulayu ndipo. Munthu amene ali ndi cha umzika zikumangotenga mphindi zitatu kuti amulembe m’kaundula wa voti.

Mkulu okuyang’anira ntchitoyi, a Alfred Kazembe, ati kuyambira pamene malowa anawatsegula loweruka lapitali, chiwerengero cha anthu amene akubwera kudzalembetsa mayina awo m’kaundulayi chakhala chikukwera.

“Mwachitsanzo dzana, kunabwera anthu okwana 175, dzulo kunabwera anthu okwana 186 ndipo lero tikuyembekezeranso kuti chiwerenero cha anthu chikwera” anatero a Kazembe.

Gawo lachiwiri la ntchito yolemba maina mkaundula wa voti ikuchitika ku maboma a Blantyre, Zomba, Thyolo, Ntcheu, Kasungu, Dowa, Mchinji, Rumphi, Nkhata-bay ndi Likoma ndipo adzatseka Lachisanu sabata ya mawa pa 22 November 2024.

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Malawi to benefit from IEA summit on clean cooking in Africa

Blessings Kanache

‘Enock Chihana apepese’

Olive Phiri

Apolisi amanga msodzi yemwe anakhapa munthu pofuna kukhwima

Davie Umar
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.