A polisi ati katswiri opima matupi aanthu, Charles Dzamalala, watsiriza kupima matupi a anthu omwe afa atamwa mowa wina kwa Manase ku Blantyre.
Mneneri wa apolisi mchigawo chakummwera, Joseph Sauka, wati zotsatirazi azitulutsa nthawi ina iliyonse.
A Sauka ati anthu asanuwa anamwalira mmodzi mmodzi atamwa mowawu, zomwe zinachititsa achipatala kuyamba ayimitsa kuti awiri mwa matupi a anthuwo asawaike mmanda kuti awapime kaye.
Anthu omwe anamwa mowawu, malinga ndi a Sauka, analipo asanu ndi atatu ndipo awiri ali mwakayakaya pomwe mmodzi akuwonetsa kusintha.