Inkosi ya Makhosi M’mbelwa V yati aMalawi akuyenera kupewa m’chitidwe wa ziwawa chifukwa dziko lino limakonda mtendere.
Inkosiyi imayankhula izi pa mwambo wa Umthetho ku Hora m’boma la Mzimba.
Mfumuyi inalangizanso zipani zonse za ndale ndi owatsatira, pamene masiku azisankho aluyandikira, kuti apewe ndale zonyozana chifukwa sizingamange dziko lino.
Mfumuyi inatinso iyi ndi nthawi yomwe aMalawi akuyenera kugwirana manja poonetsetsa kuti m’fundo zomwe boma linalonjeza zikukwaniritsidwa.
Olemba: Jackson Sichali