Bungwe la Chiwalo Youth Network lalangiza achinyamata a m’boma la Phalombe kuti athandize kulimbikitsa ukhondo m’makomo mwawo komanso m’malo a boma monga ku Polisi ndi ku chipatala.
Wapampando wa bungweli, a Patrick Makwale, ndi amene ananena izi pamene achinyamata ena amagwira ntchito yosesa pa chipatala cha boma cha Nambazo komanso Polisi ya Nambazo m’bomalo.
A Makwale anati ndi okondwa poona kuti achinyamata ambiri ku Phalombe akuonetsa chidwi pa ntchiito za chitukuko, potukula miyoyo yawo komanso ntchito za boma.