Ntchito yosindikiza ma Passport tsopano iyambanso mawa lachitatu ku Blantyre, Nthambi yoona zolowa ndikutuluka m’dziko muno, ya Immigration, yatsimikiza zimenezi.
Mneneri wa nthambiyi, a Wellington Chiponde, ati anthu onse ofuna ziphaso zoyendera, tsopano atha kuyamba kupita ku likulu la nthambiyi ku Blantyre kukapeza ziphasozi kuyambira tsikuli.
A Chiponde athokoza anthu m’dziko muno kamba kopilira pa nthawi imene nthambiyi imakonza zinthu kuti ziyambenso kuyenda bwino.
Anthu ofuna ziphaso akhala akumakatenga ziphasozi ku Lilongwe a Immigration atasiya kusindikiza ku Blantyre atathetsa mgwirizano ndi kampani yomwe inkapanga ziphasozi mmbuyomu.