Nduna ya zofalitsa nkhani yomwenso ndi mneneri wa boma, a Moses Kunkuyu akuchititsa msonkhano wa atolankhani ku Lilongwe pa lipoti la ngozi ya ndege yomwe inapha yemwe anali wachiwiri kwa mtsogoleri wadziko lino Dr. Saulos Chilima ndi anthu ena asanu ndi atatu.
A Kunkuyu ati achititsa msonkhanowu pofuna kupereka uthenga omwe uli mu lipotili muchiyankhulo chomwe anthu onse mdziko muno angamvetse chomwe ndi Chichewa.
Kampani yomwe inachita kafukufuku wa chomwe chinachititsa ngoziyi ya German Federal Bureau of Aircraft Accident Investigation (BFU) inatulutsa lipoti loyambilira la ngoziyi lachisanu pa 31 August.
Pakadali pano ndunayi ikuwerenga lipotili lomwe alitanthauzira mchichewa.