FDH Bank yapeleka chimanga chokwana matani 100 ku bungwe la National Food Reserve Agency (NFRA).
Mkulu wa zamalonda ku Banki ya FDH, a Levie Nkunika, wati achita izi potsatira pempho la mtsogoleri wa dziko lino loti dziko lino lili pa ngozi yanjala.
M’mawu ake, mkulu wa bungwe la NFRA, a George Macheka, wati ndikofunika kugwiranamanja pa ntchito yothandiza mabanja amene akhudzidwa ndi njala m’dziko muno.
Malinga ndi NFRA, dziko lino likufunika pafupifupi ma tani 200,000 kuti lithane ndi vuto lanjara.