Bungwe la Football Association of Malawi lero lapepesa ku Goshen Trust, yomwe imathandiza mpira wamiyendo wa atsikana, kaamba kochedwa kudzaonetsa chikho cha COSAFA chomwe timu ya Scorchers inapambana.
Mtsogoleri wabungwe la FAM, a Fleetwood Haiya, amayankhula mumzinda wa Lilongwe pomwe Goshen Trust imapereka K21 miliyoni, kukwaniritsa lonjezo lathumba landalama zothandiza mpira wamiyendo wa atsikana mdziko muno.
A Haiya atsutsanso mphekesera zomwe akuti zimamveka kuti bungweli silikufuna kukhalanso mu mgwirizano ndi Goshen Trust.
Poyankhulapo, mwini wa bungweli Prophet Shepherd Bushiri anati anali odabwa kaamba koti pa othandiza pampirawu sadawerengeredwe panthawi yomwe timu ya Scorchers inapambana chikho cha COSAFA.
“Ngakhale ife tinathandiza timuyi, tinaona kuli zii! Nde tinangoti kapena mwina ndichikondi chankhwangwa chifukwa izi zinachitikanso 2016,” anadandaula Bushiri.
Pamapeto pa zonse, mbali ziwirizi zinatsimikizira anthu kuti zakonza zotsamwitsa zomwe zinalipo ndipo FAM inathokoza pa thandizo la ndalama lomwe Goshen yapereka.


