Prezidenti wa dziko la Tanzania Samia Suluhu Hassan apempha maiko a mu Africa kuti apitilize kugwirizana, poti kutero kuthandiza kutukula Africa.
Mtsogoleriyu wanena izi pa mwambo wa chikondwelero choti patha zaka makumi asanu ndi limodzi (60) chikhazikitsire dziko la Tanzania kuchokera pa mgwirizano wa maiko a Tanganyika ndi Zanzibar.
Chikondwelerochi chachitika pa bwalo la za masewero la Uhuru, mkatikati mwa mvula yochuluka yomwe ati yakhala ikugwa kwa sabata imodzi.
Atsogoleri a maiko osiyanasiyana, kuphatikizapo Wachiwiri kwa Mtsogoleri wa dziko la Malawi Dr Saulos Chilima, anali nawo pa mwambowu.
A Malawi ena amene anali ku chikondwelerocho ati zawakumbutsa momwe zinalili zaka zam’buyomu ku Malawi pa zikondwelero za ufulu odzilamulira.
“Zandikumbutsa rally ku Kamuzu Stadium. Anthufe zochita zathu ndi zofanana,” Atero a Emmanuel Mphalale aku Blantyre.
Pa chikondwelerocho panali ma Prezidenti a maiko a Comoros, Namibia, Zambia, Burundi, Somalia, DRC ndi Kenya.
Waimira dziko la Mozambique anali nduna yao yaikulu – Prime Minister, pamene ku Zimbabwe ndiku Rwanda anatsogolera alendo a maikowo anali nduna zoona za maubale awo ndi maiko ena.
Kunalinso anthu ochoka ku maiko akunja kwa Africa.