Apolisi m’boma la Balaka anjata a Paul Lipenga, 46, powaganizira kuti anaononga komanso kuba nthambo za magetsi za ESCOM.
Ofalitsa nkhani pa polisi ya m’boma la Balaka, a Gladson M’bumpha, wati a Lipenga anapalamula mlanduwo pa 22 November chaka chino pa sitolo za pa Mbera m’bomalo.
A M’bumpha anati anthu ena akufuna kwabwino ndiwo anatsina khutu apolisiwo zokhuza nkhaniyi.
Apolisi atachita kafukufuku anapeza Lipenga ali ndi nthambo za ESCOM zotalika mamita 300 za ndalama zoposa K5 million.
Pakadali pano, apolisiwa ati ndi okhutira ndi momwe akugwilira ntchito pamodzi ndi anthu m’bomalo maka pofuna kuthetsa umbanda ndi umbava.
Olemba: Alufeyo Liyaya