Malawi Broadcasting Corporation
Development Local Local News

Awali ampatsa chilango

A Bester Awali, omwe ndi Phungu wa Chipani cha Democratic Progressive (DPP) wa dera la pakati m’boma la Zomba, awagamula kuti asadzapezeke pa nkumano wa komiti ya Nyumba ya Malamulo kwa masiku khumi (10) kaamba koponya botolo la madzi kwa a phungu a mbali ya boma nthawi imene kunali zokambirana dzulo m’nyumbayi.

Sipikala wa nyumbayi, a Catherine Gotani Hara ati poyambilira iwo adakonza chilango chokhwima zedi, koma adachepetsa popeza a Awali ndi akuluakulu ena a m’chipani cha DPP anapepesa poonetsa khalidwe loyipa.

Padakali pano, a Hara achenjeza aphungu onse kuti adzawapatsa chilango ngati adzachite m’chitidwe ochotsa ulemu wa Nyumba ya Malamulo.

#MBCDigital
#Manthu

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Self Help Africa empowers farmers

Sothini Ndazi

Mabanker ndi Manoma : Wamkulu ndani?

Emmanuel Chikonso

PRE BUDGET CONSULTATIVE MEETING UNDERWAY IN LILONGWE

McDonald Chiwayula
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.