Mlembi wa mkulu wa chipani cha MCP a Eisenhower Mkaka wati dziko la Malawi ladala chifukwa liri ndi mtsogoleri wa masomphenya.
A Mkaka anena izi ku mwambo okondwelera kuti bungwe la NEEF lakwanitsa kubwereketsa ngongole zokwana K100 billion.
Mlembiyu wati Dr Chakwera wayambitsanso sitima yofika ku Lilongwe patatha zaka 21 sitima-yi itasiya, ndipo kubweranso kwa mayendedwe apa njanji kuthandiza kuti ngongole za NEEF zipindulire anthu m’dziko muno.
Iwo ati n’chifukwa chake anthu a kwa M’baluku ku Mangochi kwa nthawi yoyamba asankha khansala wa chipani cha MCP.
Olemba: Blessings Cheleuka