Apolisi ku Mulanje amanga anthu asanu powaganizira kuti atentha ndi moto khola la ng’ombe komanso nyumba ati pobwezera kuphedwa kwa m’bale wawo, yemwe anthu okwiya amupha pomuganizira kuti amafuna kuba ng’ombe.
Izi zachitika pamudzi wa Nguwo, mfumu yaikulu Juma m’bomali. Ofalitsankhani wapolisi ku Mulanje, Innocent Moses, wati mchimwene wa anthuwo, Rashid Chingwalu wazaka 40 anapita mmudzimo komwe amakakambirana zokhudza banja.
Kenako madzulo anapita pamalo ena omwera mowa mpaka 10 koloko usiku. Chingwalu anapita pamalo ena kuti akadzithandize pafupi ndi khola la ng’ombe.
Mwini kholalo atawona izi anaitana anthu poganiza kuti munthuyo ndi mbava ndipo anthu okwiya anagwira Chingwalu ndikumupha.
Malinga ndi a Moses, abale a malemuwo anapita ku polisi ya Namphungo ku Mulanje kukafotokoza zakuphedwa kwa m’bale wawoyo.
A Moses ati anthuwo sanakhutitsidwe ndi zomwe apolisiwo anawauza kuti afufuza za nkhaniyo. Kenako anthuwo analunjika kwa mwini khola la ng’ombezo ndikutentha kholalo komanso nyumba yake.
Iwo anapitilira ndi chipwirikiti mpaka pomwe apolisiwo anawamanga.