Wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino Dr Michael Usi ali nawo pa zochitika zokhazikitsa bungwe la Malawi Church and Community Transformation Movement m’chigawo cha kum’mwera.
Bungweli ndi lopangidwa ndi atsogoleri amipingo ndipo lidzigwira ntchito ndi mafumu komanso anthu osiyanasiyana.
Cholinga chake ndi kulimbikitsa ntchito zabwino m’magawo osiyanasiyana a chitukuko.
Dr Usi anayenda nawo pa ulendo wa ndawala kuchoka ku HHI mpakana pa mpingo wa Word Alive International Ministries munzinda wa Blantyre.