Apolisi mchigawo chakummwera ati tsopano ayamba kumanga anthu onse omwe akugulitsa mowa owopsa wa ‘ambuye tengeni’ omwe waphetsa anthu asanu kwa Manase ku Blantyre.
Anthu ena atatu ali m’chipatala.
Mneneri wa a polisi mchigawochi, a Joseph Sauka, ati apolisi ali kale mmadera osiyanasiyana komwenso akulanda mowawu, omwe ati ndi owopsa kwambiri.
“Cholinga chathu ndikuteteza anthu ku imfa zodza kamba kakumwa mowa osavomerezeka, omwenso ndi owopsa,” atero a Sauka.