Dr Micheal Usi, amene ndi wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino, ati achita zotheka polimbikitsa chipani cha UTM, monga mtsogoleri wachipanichi, kuti chikhale champhamvu.
Iwo ati cholinga chawo ndikukwaniritsa masomphenya a yemwe anali wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino, malemu Dr Saulos Chilima.
Dr Usi anena izi pamene amacheza ndi anthu a kumudzi kwawo kwa Golden kwa mfumu yaikulu Chikumbu m’boma la Mulanje.
Iwo atsimikiziranso anthu a m’boma la Mulanje kuti boma ladzipereka potukula miyoyo yawo, kuphatikizapo kupereka ngongole kwa ochita bizinezi.