Mtsogoleri wa dziko lino, Dr Lazarus Chakwera, wamema anthu amene amayendetsa ntchito zosamalira anthu kuti asamakondere pa ntchito monga za mtukula pakhomo.
Dr Chakwera anapemhanso anthu amene amagawa chakudya kwa amene akhudzidwa ndi njala kuti asamakondere pogwira ntchito.
Iwo amayankhula kwa anthu amene anasonkhana pa Jenda m’boma la Mzimba pamene mtsogoleri wadziko linoyu akupita m’chigawo cha kumpoto.
Mtsogoleri wa dziko linoyu anati boma lake ladzipereka kuonetsetsa kuti anthu akhale ndi madzi abwino.
Wachiwiri kwa mlembi wamkulu wa chipani cha Malawi Congress, a Catherine Gotani Hara, phungu wadera lakumwera m’boma la Mzimba, a Emmanuel Chambulanyina Jere komanso Inkosi Mabilawo anayamika boma kaamba ka ntchito za chitukuko zimene zikuchitika posakondera chigawo.
Iwo anatchulapo ntchito ya mtukula pakhomo imene ikuthandiza mabanja ambiri ndi madzi abwino amene ali ku Luwerezi.
Iwo anathokozanso kaamba ka nyumba khumi za apolisi pa Jenda zimene zatha kale komanso zina zimene zikumangidwa ku Embangweni, sukulu ya sekondale yatsopano ku Bangalala komanso ntchiito yomanga M’mbelwa University, imene idalephereka m’mbuyomu.
Olemba: Isaac Jali