Yemwe anakhalapo wachiwiri kwa mtsogoleri wachipani cha DPP m’chigawo chapakati ndipo tsopano analowa Malawi Congress (MCP) a Uladi Mussa, apempha anthu m’dziko muno kuti akhale pambuyo pa Prezidenti Dr Lazarus Chakwera komanso chipani cha MCP, omwe akangalika kutukula dziko lino.
A Mussa amalankhula izi pa msonkhano omwe nduna yazam’dziko, a Ken Zikhale Ng’oma, achititsa pa sukulu ya Mpatsa mdera la pakati m’boma la Nsanje.
Iwo ati Dr Chakwera adzapambananso chaka cha mawa kamba ka ntchito zachitukuko zomwe zikuchitika mdziko muno.