Komishonala wa DoDMA, a Charles Kalemba, walangiza makomiti othandiza anthu kuti adziwonetsetsa kuti okhawo okhudzidwa ndi ngozi zakugwa mwadzidzidzi ndi amene akulandira thandizo.
A Kalemba anena izi pa sukulu ya sekondale ya Bwaila munzinda wa Lilongwe pamene amatsekulira maphunziro a makomiti amene amagwira ntchito zolemba mayina mu kaundula wa anthu oyenera kulandira thandizo.
“M’mbuyomu zachitikapo kuti anthu oyenera kulandira thandizo osapatsidwa koma thandizo kupita kwa anthu amene siwoyenera. Maphunziro awa cholinga chake n’kuthetsa zimenezi,” a Kalemba anatero.
Iwo anawonjezeranso kuti pamene DoDMA ikukonzekera ntchito yogawa chakudya kwa anthu ovutikitsitsa amene akhudzidwa ndi njala, nthambiyi ikulimbikitsa onse ogwira ntchitoyi kuti atsatire ndondomeko zabwino kuti onse omwe akhudzidwa ndi mavuto monga anjala komanso ng’amba athandizidwe.
Mkulu wa khonsolo ya nzinda wa Lilongwe, a McCloud Kadammanja, anati maphunzirowa athandiza kuthetsa mavuto amene analipo pa dongosolo la kalembedwe ka mayina komanso kagawidwe ka thandizo.
Bungwe la DoDMA lati posachedwapa liyamba ntchito yogawa chakudya kwa anthu amene akhudzidwa ndi njala m’madera ena a m’dziko muno.