Mtsogoleri wa dziko lino, Dr Lazarus Chakwera, wati aMalawi akuyenera kugwira ntchito molimbikira kuti dziko lino lipeze chuma.
Dr Chakwera ati zina mwa ntchito zimene zikugwiridwa m’dziko lino zikutheka kaamba kaubale wabwino umene ulipo pakati pa dziko la Malawi ndi la Mozambique, kudzera mwa mtsogoleri wa dzikolo, Dr Filipe Jacinto Nyusi.
Dr Chakwera atinso kudzera mu ulimi, dziko lino litukuka maka likatsatira njira zamakono zaulimi.
Iye amayankhula potsekulira chionetsero cha malonda a zaulimi, pamodzi ndi Dr Nyusi, mu mzinda wa Blantyre.