Malawi Broadcasting Corporation
Development Local Local News Nkhani

Malemu Lapukeni awayika lero

M’mawa uno, nduna yofalitsa nkhani, a Moses Kunkuyu, anali nawo pa mwambo operekeza maliro a Abdul Lapukeni kuchoka munzinda wa Lilongwe.

A Lapukeni, omwe ndi m’modzi mwa omwe adachita ngozi ya ndege imene munali wachiwiri kwa mtsogoleri wadziko lino, malemu Dr Saulos Chilima, awayika m’manda lero kumudzi kwawo m’boma la Mangochi pofuna kulemekeza mwambo wa maliro a chipembedzo cha chisilamu.

Achibale komanso anthu okhudzidwa anasokhana nawo ku Sunset Funeral Parlor.

Malemu Lapkeni anali m’modzi mwa akuluakulu ku unduna owona zakunja kwadziko lino.

Matupi a anthu asanu ndi awiri, kuphatikizapo thupi la Malemu Lapukeni, ndiomwe anawasunga pa nyumba ya chisoni ya Sunset parlor ku Lilongwe.

Olemba: Margaret Mapando

 

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

WHERE IS K10 TRILLION? FND DEMANDS PROBE

MBC Online

Wanderers secure second place

Romeo Umali

OVER 20 US SURGEONS COMING TO MALAWI FOR FREE CARDIAC OPERATIONS

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.