Malawi Broadcasting Corporation
Nkhani

‘Chilungamo pa malonda ndichofunika’

Bungwe la Malawi Bureau Standards (MBS) lati kugwira ntchito limodzi ndi nthambi zina zaboma nkofunika pa ntchito zolimbikitsa chilungamo pa malonda, mwazina.

Mkulu wa bungweli, a Ben Thole, anena izi pa mkumano omwe MBS linakonzera apolisi komanso owona za malonda m’makhonsolo am’chigawo chakumpoto.

A Thole ati ndi cholinga cha MBS kuonetsetsa kuti pali chilungamo pa malonda komanso kuti amalonda akugwiritsa ntchito milingo yoyenelera pogulitsa malonda awo.

“Tikufuna amalonda adzigulitsa katundu wa mulingo komanso muyeso oyenelera, zonsezi nzothandiza kuti anthu akugula katundu oyenelera komanso otetezedwa,” walongosola Thole.

Mikumano yotere yachitika kale m’zigawo zakummwera ndi pakati.

Olemba: George Mkandawire

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Tikambe zabwino za dziko lathu — JB

MBC Online

Wapereka mimba kwa mwana wobereka yekha

Charles Pensulo

Alimi ayamikira mitengo ya fodya

Mayeso Chikhadzula
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.