Wachiwiri kwa Mtsogoleri wa dziko la Iran a Mohammad Mokhber nde mtsogoleri watsopano wa dzikoli kutsatira imfa ya mtsogoleri wawo a Ebrahim Raisi pa ngozi ya ndege.
Malinga ndi gawo 131 la malamulo oyendetsera dzikoli, a Mokhber akuyenera kugwira ntchito ndi akulu akulu a nyumba ya malamulo komanso akulu akulu owona malamulo pokonzekera chisankho cha President chomwe chichitike m’masiku osapyola makumi asanu.