Chipani cha UTM chalengeza ganizo lake lofuna kuchoka mu mgiwirizano wa Tonse Alliance.
Akuluakulu a chipanichi ndiwo anena izi lero kumsonkhano wa atolankhani umene achititsa munzinda wa Lilongwe.
Ena mwa akuluakulu amene ali pamsonkhanowo ndi mlembi wamkulu wa chipani chi, a Patricia Kaliati komanso mneneri wachipanichi, a Felix Njawala.
Mwazina, a Kaliati ati nkumano omwe anali nao umayenera kukhalapo potengera kuti chimwalireni mtsogoleri wa chipanichi Dr Saulos Chilima sanakhale nao.
Pazachilinganizo chotuluka mu mgwirizano wa Tonse, iwo ati ganizo lotsimikizika adzapereka pa nkumano wa pa 19 July mwezi uno.
Zipani zinanso zimene zili mu mgwirizanowu ndi monga People’s Party komanso MAFUNDE.