Anthu amunzinda wa Blantyre anali okondwa kwambiri ataonelera maimbidwe ochititsa chidwi kuchoka kwa oimba wa chamba cha amapiano, Young Stunna, wochokera m’dziko la South Africa.
Mwambowu unali wachiwiri a Beerland and Classic Events atawukonzanso Young stunna atalephera kubwera m’mwezi wa May chaka chino.
Ena omwe anaimbanso kumwambowu anali Kell Kay, Eli Njuchi, Zeze Kingston, Tuno komanso Fada Moti.
Olemba: Andrew Lambulira