Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

Bwezani ngongole kuti ena apindule — NEEF

Bungwe la National Economic Empowerment Fund (NEEF) lati zomwe anthu ena akufalitsa kuti boma lakhululukira onse omwe anatenga ngongole ku NEEF kuti asabweze ndi zabodza.

Kotero mkulu wa bungweli, a Humphreys Mdyetseni, walimbikitsa mafumu, aphungu a nyumba ya malamulo, makhansala komanso atsogoleri a komiti ya chituku cha kumudzi (Area Development Committee) kuti akhale patsogolo kulimbikitsa komanso kukumbutsa anthu mmadera awo kuti adzibweza ngongole yomwe anatenga ku bungweli kuti enanso apindule.

Bungwe la NEEF limakumana ndi adindo ochokera ku Nkhoma ndi Mitundu m’boma la Lilongwe, kumene akuti kuli chiwerengero chokwera cha anthu amene akuvuta kubweza ngongole.

Ena mwa adindo amene anali nawo pa mkumanowu ndi T/A Kalumbu, T/A Chadza, T/A Masula, phungu wa Lilongwe Mpenu-Nkhoma komanso a Baba Steven Malondera, phungu wa Lilongwe South East.

“Tikuyenera kuwonetsetsa kuti anthu akutsatila zomwe anagwirizana ndi bungwe la NEEF,” atero a Kalumbu.

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Gaborone United, UWC in CAF Qualifiers final

MBC Online

Mwaungulu tsopano adzivala Jersey 11

Romeo Umali

NAMIWA FOUND

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.