Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

‘Dekhani pa bizinesi’

Achinyamata omwe alandira mpamba wa ndalama zokwana K1 million aliyense kuchokera kwa Triephornia Mpinganjira pansi pa ndondomeko ya ‘kuthandiza omwe alibe kuthekera kupita patsogolo’ awalangiza kukhala okhazikika pa masomphenya awo komanso kudekha pomwe tsopano akuyembekezeka kuyamba bizinesi zawo.

Nkhalakale pa ntchito za malonda mdziko muno, Napoleon Dzombe komanso Mayamiko Mkoloma omwe anaitanidwa kudzafotokoza mbiri yawo ngati chilimbikitso kwa achinyamatawa ndiomwe apereka malangizowa.

Mkoloma yemwe ndiwachinyamata yemwe ali ndi kampani yaikulu ya Imosys wati chiyambi chimakhala chovuta pomwe bizinesi zimakumana ndimabvuto osiyanasiyana zomwe zimafunika kudekha komanso kukhazikika pa loto lomwe ukufuna kukwaniritsa.

Ndipo nawo a Dzombe, analimbikitsa achinyamatawa ndikuwachenjeza zopewa kuthamangira kuyamba kusangalala ndikuononga mpamba wa bizinesi zawo zisanakhazikike.

“Lero mwalandira mbewu chonde kabzaleni ndipo mudzakolola,” anatero a Dzombe omwe ndi mkulu wa Mtalimanja holdings komanso katswiri pa ulimi.

Mmodzi mwa achinyamata omwe alandira mpambawu, Hawa Shabir wati awonesetsa kuti loto lake likwaniritsidwe.

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

MBC gets its turn at Parliament

Trust Ofesi

Chibuku supports Queens with K2 million

MBC Online

PARLIAMENT PASSES MID YEAR BUDGET REViEW

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.