Malawi Broadcasting Corporation
Agriculture Business Development Local Local News Nkhani

Ulimi wa nkhuku ndiothandiza

Mawanja oposa makumi awiri ku Choma mu mzinda wa Mzuzu ati ali ndi chiyembekezo kuti ulimi wa nkhuku omwe bungwe la SOS lawathandiza uli ndikuthekera kotukula miyoyo yawo.

Mawanjawa lachiwiri alandira nkhuku 2,000 komanso chakudya cha nkhukuzi zomwe ndi za ndalama zoposa 30 million Kwacha.

Polankhula ndi MBC, mmodzi mwa opindula ndi ndondomekoyi mai Dorica Shaba omwe ali ndi ana anai ati thandizoli lawapulumutsa kumavuto omwe amakumana nao.

“Ndinali pa mavuto ambiri monga kupeza chakudya, zovala komanso zinthu zofuna ana anga kusukulu, kaamba koti ndinalibe ondithandiza koma kubwera kwa SOS ndithu ndaona zithu zambiri zasintha,” watero Shaba

Mai Shaba akuti panopa nkhuku ndi chakudya chake chomwe alandira ziwathandiza kwambiri zikakula pomwe agulitse kupeza ndalama komanso manyowa kuchokera ku zitotsi zake.

Nao a Kenneth Singini omwe ali ndi ana awiri ati thandizo lomwe alandilari lisintha kwambiri banja lao pa chuma ndi nkhani zakadyedwe kabwino.

Mmau ake mkulu oyendetsa ntchito za bungwe la SOS ku Mzuzu a George Kondowe ati ntchitoyi yangoyamba ndipo akuyembekezeka kugawa nkhuku 5,000 ku mawanja oposa 200.

“Ntchito yopereka nkhukuyi ndi ya ndalama zoposa K30 million kwacha ndipo tigawanso Mbuzi, Nkhumba ndi zina zambiri zomwe zonse pamodzi ndu za ndalama zokwana 100 million kwacha,” walongosola Kondowe

Kondowe wati cholinga chachikulu cha ndondomekoyi ndikuthandiza mawanjawa kukhala odzidalira pa chuma komanso kuthandiza kuti ana adzipita kusukulu ndikukhala malo abwino.

Olemba : George Mkandawire
#MBCDigital
#Manthu

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Malawi, Nigeria push Airtel Africa to a loss

Justin Mkweu

WLA CONDUCTS LEGAL CLINICS, DONATES TO CYCLONE FREDDY SURVIVORS

McDonald Chiwayula

NAMADINGO PENS AMBASSADORIAL DEAL WITH FDH

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.