Bungwe loona zachakudya padziko lonse la FAO lati lipitiriza kugwila ntchito ndi dziko la Malawi powonetsetsa kuti boma likwaniritse masomphenya ake owonetsetsa kuti anthu ali ndi chakudya chokwanira.
Mkulu wa bungweli Qu Dongyu wanena izi atachita zokambirana ndi Prezidenti Dr Lazarus Chakwera ku likulu la bungweli ku Rome mdziko la Italy.
Mmau ake, Dr Chakwera anati boma lake likutsata mfundo zolimbikitsa ulimi, zokopa alendo komanso zamigodi pofuna kukweza dziko ndi miyoyo ya a Malawi.
Iwo anati anthu pafupifupi 5.5 million akufunika thandizo la chakudya mdziko la Malawi kaamba ka ng’amba yomwe inagwa m’maboma ambiri.
Pa chifukwachi a Dongyu ati agwira ntchito ndi boma la Malawi pothandiza anthu omwe akuvutika.