Malawi Broadcasting Corporation
Development Local Local News Nkhani

‘Boma lithandiza onse’

Wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino, Dr Michael Usi, wati boma likuyesetsa kuti anthu onse amene akhudzidwa ndi njala akhale ndi chakudya posatengera dera limene akukhala komanso kusiyana pandale .

Dr Usi ayankhula izi m’boma la Chiradzulu pamene amagawa chimanga kwa mabanja amene akhudzidwa ndi njala m’dera la phungu wa chipani chotsutsa cha Democracy Progressive (DPP), a Joseph Mwanamvekha.

“Bomali ndi la aliyense ndipo lipitilira kuthandiza onse,” anatero Dr Usi.

A Mwanamvekha anayamikira wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko linoyu kaamba ka thandizo limene apereka ndipo iwo ati njala ndi yayikulu mdera lawo.

Ena mwa anthu amene alandira thandizoli ndi mabanja amene anasamuka kuchokera m’mudzi wa Ntauchira omwe unakokoloka ndi Namondwe wa Freddy.

Mfumu Mussa ya pamudzi wa tsopanowu inayamikiranso boma powafikira ndi thandizo la chakudya.

Pa mwambo ogawa chimangawu, Dr Usi anadzudzulanso mchitidwe wochitana chipongwe kaamba kosiyana zipani.

Olemba: Mercy Zamawa

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

MEC ichititsa chisankho chakhansala ku Chilaweni mwezi wa mawa

MBC Online

Five arrested for murder in Mzimba

MBC Online

Government plans to allocate 200,000 hectares for irrigation farming

Beatrice Mwape
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.