Unduna wa za ulimi wakhazikitsa ntchito yopereka feteleza wangongole kwa alimi a m’ma boma a Chikwawa ndi Nsanje.
Ntchitoyi ili pansi pa bungwe la National Economic Empowerment Fund (NEEF).
Nduna ya za ulimi, a Sam Kawale, ayankhula izi pamwambo okhazikitsa ntchitoyi mdera la mfumu yayikulu Maseya m’boma la Chikwawa.
A Kawale ati ndondomeko yopereka feteleza pangongoleyi ndi chiyambi chosintha ntchito za ulimi kuti zikule mpakana alimi atafika pomagwiritsa ntchito zinthu monga ma thalakitale polima.
Mkulu wa NEEF, a Humphrey Mdyetseni, anati pofika lero apereka feteleza kwa alimi pafupifupi 36,000.
Polankhula ku Nsanje, mfumu yaikulu Mlolo yalimbikitsa alimi opindula kuti agwiritse bwino ntchito fetelezayu komanso akumbukire kubwenza ngongole.
Ntchito yogawa feteleza m’ma bomawa inayamba miyezi ingapo yapitayo.