Unduna owona zachisamaliro cha anthu wati ndiokhumudwa kuti anthu achikulire akupitilira kuphedwa ndi kuchitiridwa nkhanza mdziko muno ngakhale kuti malamulo oletsa mchitidwewu alipo.
Nduna yaona zoti pasamakhale kusiyana pakati pa amayi ndi abambo ndi chisamaliro cha anthu, a Jean Sendeza yanena izi mnyumba ya malamulo poyankha funso la phungu wa dera la Zomba Lisanjala, a William Susuwele Banda omwe anadandaula za kuchuluka kwa nkhanza zomwe achikulire akukuchitiridwa mdziko muno.
A Banda ati kuyambira January chaka chino anthu achikulire okwana 18 aphedwa mdziko muno kaamba kowaganizira za ufiti.
Nkuyankha kwao, a Jean Sendeza adandaula kuti anthu ambiri omwe akumachitira nkhanza achikulirewa sakumalandira chilango chokhwima komanso
nkhanizi zikungochuluka mmakhoti ndipo milandu yake ikumatenga nthawi kuti ayiweruze.
Apa ndunayi yati kudzera mu lamulo la tsopano lomwe layamba kugwira ntchito pa 16 September chaka chino, iwo awonetsetsa kuti akugwira ntchito mogwirizana ndi apolisi ndi adindo ena kuti vutoli lithe.