Bwalo lamilandu ku Lilongwe lalamula mwamuna wazaka 51, Ndaona Kabango, kukakhala ku ndende zaka 19 chifukwa chokhapa mkazi wake wazaka 46, Charity Kamumayani, ndi chikwanje komanso kudula zala zake ziwiri za kumapazi.
Mneneri wapolisi ku Lilongwe Hastings Chigalu wati mwamunayo anauza amayi omwe anali pamwambo wa chinamwali kuti tsikulo linali lomaliza kumuona mkazi wake wakaleyo, yemwe anasiyana naye chaka cha 2021.
Kenako madzulo ake, mwamunayo anatenga chikwanje kuyamba kuthamangitsa mkazi wakeyo, yemwe amachokera kwa a malume ake amwamunayo kumene amakadandaula kuti mwamunayo akumuopseza kuti amupha.
Ali mkati momuthamangitsa, mkaziyo anagwa ndipo Kabango anapeza mpata womukhapa.
Kukhoti, mwamunayo anapempha kuti amukhululukire kaamba koti akufuna kubwelerana ndi mkazi wakeyo kuti adzilera limodzi ana awo awiri koma khotilo lakana izi ponena kuti mkaziyo walumala kaamba ka mwamunayo.