Boma lasintha alembi ena muma unduna
Boma lasintha maundindo a alembi akulu a maunduna ena.
M’neneri mu ofesi ya mlembi wa mtsogoleri wa dziko lino ndi nduna zake, a Robert Kalindiza, atsimikiza za nkhaniyi.
Ena mwa anthu amene asinthidwa ndi awa: a Chikumbutso Mtumodzi amene anali m’modzi mwa akuluakulu ku unduna wazofalitsa nkhani pano ndi mlembi wamkulu ku unduna wa zachinyamata, a Hetherwick Njati amene anali mlembi wamkulu ku unduna wazofalitsa nkhani pano apita ku unduna wazachuma, a Chikondano Mussa amene anali mlembi wamkulu ku unduna wa zamaphunziro pano ndi mlembi wamkulu ku unduna owona za ogwira ntchito.
A Kalindiza ati kusinthaku sikwachilendo ndipo kukugwirizana ndi masomphenya a mtsogoleri wa dziko lino Dr. Lazarus Chakwera owonetsetsa kuti maunduna akugwira ntchito mokomera a Malawi.