Wachiwiri kwa nduna yaza ulimi Benedicto Chambo anacheza ndi akuluakulu achipembezo chachi Rasta munzinda wa Lilongwe.
A Chambo, omwenso ndi phungu wadera la Mangochi – Makanjira, ati ma rasta ndi anthu ofunikira kwambiri pa chitukuko cha dziko lino choncho akufunika osamawssiya mmbuyo pokwaniritsa masomphenya a Malawi 2063.
Iwo ati ichi ndichifukwa chake mtsogoleri wa dziko lino amaonetsetsa kuti aliyense adzitha kukhala ndi mwayi okhala m’maudindo osiyanasiyana ofunikira.
Ras elder Mwanamanga, yemwenso ndi mmodzi mwa atsogoleri ku mpingo wachi Rasta Ku Nyabingi House ku Area 17 munzinda wa Lilongwe, wati ndi okondwa kuti boma layika padera mapologalamu osiyanasiyana omwe cholinga chake nkusintha miyoyo ya anthu m’dziko muno.
Lachisanu pomwe aphungu amamaliza msonkhano wawo, ma rasta anali nawo kunyumbayi kutsatira zokammbiranazi.