Malawi Broadcasting Corporation
Local Local Nkhani

Anthu aku Mangochi akondwa ndi kusindikiza zitupa zoyendera

Anthu ambiri m’boma la Mangochi ndi maboma ena a m’chigawo cha kumvuma akondwera ndi kuyambanso kwa ntchito yopanga zitupa zoyendera zomwe ikuchita nthambi ya Immigration m’bomali.

Polankhula ndi MBC ku ofesi ya nthambiyi ku Mangochi, anthuwa ati kuyambanso kwa ntchitoyi kuchepetsa mavuto ena omwe amakumana nawo monga kuyenda ulendo wa utali kukafika ku Lilongwe kapena ku Blantyre kuti apangitse zitupa zawo.

Mayi Esther James a m’boma la Machinga anati “ife nkhani imeneyi tayilandira bwino kuno, timangomva kuti ntchitoyi iyamba posachedwa kuno ku Mangochi koma tsopano takhulupilira.”

Pothilirapo ndemanga, a Victim Chilanga, amene amachokera m’dera la Mfumu Yaikulu Nankumba m’boma la Mangochi anati adachedwa kupangitsa passport chifukwa mtunda umatalika kukafika mu mzinda wa Lilongwe.

Ofalitsa nkhani ku nthambi ya Immigration ya m’chigawo cha kumvuma, a Edward Chidzalo, ati ofesi yawo ikupanga ndondomeko zofunikila zomwe anthu amayenera kutsata akafuna kupangitsa chitupa choyendera.

Koma a Chidzalo anati ntchito yosindikiza ikuchitikila ku ofesi ya Lilongwe.

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

163,000 candidates to write JCE this year

Chisomo Break

Sports is a risk-deterrent — Lumbadzi Police

Romeo Umali

Super League action returns!

Sothini Ndazi
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.