A Ken Msonda, omwe alandiridwa ku chipani cha Malawi Congress MCP dzulo, ati ndi odabwitsidwa ndi chilimbikitso chimene apatsidwa ndi mafumu akuluakulu a m’boma la Rumphi pamene alowa m’chipanichi.
Iwo ati sizinachitikepo mu mbiri ya ndale m’dziko muno mafumu kuperekeza munthu kukalowa chipani.
Polowa m’chipani cha MCP, a Ken Msonda anaperekezedwa ndi mafumu motsogozedwa ndi Paramount Chief Chikulamayembe komanso m’busa Victor Chikhosa wa mpingo wa Chiweta CCAP, mwa ena.
“Ambuye watseka pakamwa onse wotukwana, wolalata, wonyoza,” atero a Msonda.
By Blessings Cheleuka