Bwalo lamilandu ku Balaka lalamula a Phutheya Galeta azaka 70 kuti akagwire ndende yakalavula gaga kwa zaka 14 chifukwa chochita zadama ndi mwana.
Ofalitsa nkhani za Polisi ya Balaka Gladson M’bumpha watsimikiza nkhaniyi ndipo wati a Galeta adagwilira mwanayo yemwe ndi wazaka 14 mwezi wa June,2024.
Oweluza milandu Joshua Nkhono wati wapereka chilangocho kuti ena atengerepo phunziro.
A Galeta amachokela mmudzi wa Malula kwa mfumu yaikulu Sawali ku Balaka.