Apolisi ku Dowa amanga mayi wazaka 35 chifukwa chomuganizira kuti wavulaza mwana wake wa zaka 12 ndi madzi otentha, mwanayo atadya mbatata asanapemphe mayi akewo.
Ofalitsankhani zapolisi ku Dowa, Alice Sitima, wati mayiyo, Chimwemwe Kayere, anachoka mammawa kupita kumunda ndi mwamuna wake kusiya mwanayo akugona.
Mwanayo atadzuka, anaphika mbatata yomwe inali mnyumbamo kuti adye.
Koma mayiyo atabwera kuchokera kumundako, sizinamusangalatse ndipo anaphula pamoto poto yemwe munali mbatatayo ndikumuthira mwanayo, iye ndikuthawa.
Bambo amwanayo atafika anamutenga ndikuthamangira naye kuchipatala.